Psalms 87

Salimo la Ana a Kora.

1Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;
2Yehova amakonda zipata za Ziyoni
kupambana malo onse okhalamo a Yakobo.
3Za ulemerero wako zimakambidwa,
Iwe mzinda wa Mulungu:
Sela
4“Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni
pakati pa iwo amene amandidziwa.
Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi,
ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ”

5Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti,
“Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye,
ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.”
6Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina:
“Uyu anabadwira mʼZiyoni.”
Sela
7Oyimba ndi ovina omwe adzati,
“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”
Copyright information for NyaCCL